Malawi: Vuto La Ma Pasipoti Lizatha? a Zikhale Akuti Makina Alipowo Akuchedwa, Akupanga Mapasipoti 500 Okha Pa Tsiku

18 April 2024

Nduna yoona za m'dziko a Ken Zikhale Ng'oma yati makina amene akuwagwiritsa ntchito posindikiza ziphaso zoyendera (passports) akugwira ntchitoyo mochedwa kwambiri.

Ndunayi yati makinawa akumasindikiza ziphaso zosadutsa 500 patsiku zimene zikuchititsa ntchitoyi kumagwirika mochedwa.

Iwo ati pakadali pano nthambiyi ili ndi ziphaso zofuna kusindikiza zokwana 35,000 zimene ikudikira koma apereka chikhulupiriro kuti izi zitheka posachedwapa.

A Ng'oma anena izi pamene adakayendera likulu la nthambiyi mu mzinda wa Blantyre.

Iwo ati adapeza kampani ina ya m'dziko momwe muno imene yakhala ikugwira ntchitoyi pamene akudikira kupeza ina yoti izigwira ntchitoyi mokhazikika.

AllAfrica publishes around 400 reports a day from more than 100 news organizations and over 500 other institutions and individuals, representing a diversity of positions on every topic. We publish news and views ranging from vigorous opponents of governments to government publications and spokespersons. Publishers named above each report are responsible for their own content, which AllAfrica does not have the legal right to edit or correct.

Articles and commentaries that identify allAfrica.com as the publisher are produced or commissioned by AllAfrica. To address comments or complaints, please Contact us.